Tenders

TAYAMBA KUGULA CHIMANGA CHA NKHOKWE ZABOMA 2023/24

Bungwe la Boma la National Food Reserve Agency (NFRA) likulengeza za kutsegulira kwa msika wa chimanga wa chaka chino cha 2023/24.

Bungweli likudziwitsa onse amene ali ndi chimanga kuti akhoza kukagulitsa chimanga chawo kuma Depoti a NFRA awa: Bangula ku Nsanje, Nkhokwe za Boma ku Kanengo ku Lilongwe, Nkhokwe za Boma ku Mzuzu, Kazomba ku Mzimba, Limbe ku Blantyre, Nkhokwe za Boma ku Luchenza, komanso Nkhokwe za Boma ku Mangochi.

Ofuna kugulitsa abweretse chimanga chosachepera tonne limodzi mugalimoto losatseka pamwamba (galimoto za mtundu wa van sizololedwa). Chimanga chikhale chomwe chakoloredwa kumene kapena chaka chapitachi, chosankhidwa bwino komanso chikhale ndi zochiyenereza izi:

  • Chikhale chouma bwino (chinyontho chisadutse 12.5% kuchuluka);
  • Chikhale cha mtundu oyera;
  • Chisakhale choonongeka ndi anankafumbwe kapena tizilombo tina ta mbeu;
  • Chisakhale choswekasweka kapena mphwemphwa;
  • Chisakhale ndi anankafumbwe kapena tizilombo tina tamoyo;
  • Chisakhale ndi zinthu zina zilizonse zosayenera kupezeka muchimanga;
  • Chisakhale choyamba kumera;
  • Chisakhale chowora.

Dziwani kuti NFRA idzabweza chimanga chonse chimene sichizafikira pa zochiyenereza zimenezi.

Mtengo ogulira chimanga ndi K550 pa kilogalamu ndipo NFRA ikhala ikugula chimangachi mpaka pa 30th September 2023 kapena kulekezera pamene chimanga chimene chikufunika kugulidwa chakwana. Kagulidwe kadzatengera oyamba kufika ndi chimanga ku ma Depoti a NFRA.

Ogulitsa adzalandira ndalama zawo pasadapite ma ola (hour) 48 kudzera ku banki yawo.

Ofuna kudziwa zambiri za msika umenewu alembere NFRA pogwiritsa ntchito e-mail iyi: nfra@nframw.com kapena ayimbe lamya ku manambala awa: +265 999 212 671 kapena +265 887 082 355 (356).

 

MANAGEMENT

Date: 24th May 2023

BUYING OF MAIZE FOR THE STRATEGIC GRAIN RESERVE 2023/24
SUPPLY AND INSTALLATION OF REAL-TIME STOCK MANAGEMENT SYSTEM (RTSMS) Re-advertised- October 2022 (Closed)
INVITATION FOR PREQUALIFICATION OF SUPPLIERS FOR 2022/2023 FINANCIAL YEAR (Closed)
STRATEGIC GRAIN RESERVE MAIZE PROCUREMENT (Closed)
DISPOSAL OF MOTOR VEHICLES BY OPEN TENDER - April 2022 (Closed)
Invitation for to tender - International Competitive Bidding (ICB) - Supply And Delivery Of Trough Chain Conveyor Systems (Closed)
SUPPLY AND INSTALLATION OF REAL TIME STOCK MANAGEMENT SYSTEM (RTSMS) (Closed)
Addendum - Warehouse Rehabilitation Works - March 2020 (closed)
Notification of intention to Contracts Award (Closed)
Invitation for prequalification of suppliers for 2021/2022 financial year (Closed)
invitation to tender for provision of catering services - June 2019 (Closed)
Supply and Delivery of Non Genetically Modified Organism (GMO) White Maize (Closed)
Request for Expression of Interest - (REAL TIME STOCK MANAGEMENT SYSTEM) - June 2019 (Closed)
Invitation to tender for Road and Drainage at Kanengo Silos - October 2020 (Closed)
Open tender maize intake - January 2020 (closed)
Supply and Delivery of Non Genetically Modified Organism (GMO) White Maize - August 2019 (Closed)
Pre-Qualification of Suppliers 2018 - 2019 (Closed)
Request for Expression of Interest - (HIGH PRESSURE SILOS CLEANING EQUIPMENT) - June 2019 (Closed)